Ekisodo 23:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Levitiko 20:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndipo musatsatire mfundo za mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+ Deuteronomo 12:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Samala kuti usagwidwe mumsampha wawo,+ pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso pako, kutinso usafufuze za milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inali kutumikira bwanji milungu yawo? Ndithudi inenso ndidzachita zomwezo.’ Yeremiya 10:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova wanena kuti: “Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono,+ ndipo musamaope zizindikiro zakumwamba, chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+
24 Usaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo usapange chilichonse chofanana ndi zifaniziro zawo,+ koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+
23 Ndipo musatsatire mfundo za mitundu imene ndikuichotsa pamaso panu,+ chifukwa iwo amachita zonsezi ndipo amandinyansa.+
30 Samala kuti usagwidwe mumsampha wawo,+ pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso pako, kutinso usafufuze za milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inali kutumikira bwanji milungu yawo? Ndithudi inenso ndidzachita zomwezo.’
2 Yehova wanena kuti: “Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono,+ ndipo musamaope zizindikiro zakumwamba, chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+