19 Zopereka zonse zopatulika,+ zimene ana a Isiraeli azipereka kwa Yehova, ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, ngati gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano losatha limene lidzakhala mpaka kalekale pakati pa Yehova ndi iwe ndi mbadwa zako.”+