4 Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Dziko lija ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbewu yako’+ ndi limeneli. Ndakuonetsa kuti ulione ndi maso ako chifukwa sudzawoloka kukalowa m’dzikolo.”+
2 “Mose mtumiki wanga wamwalira.+ Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu ndi kulowa m’dziko limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+