38 Wansembe Aroni anakwera m’phiri la Hora monga mmene Yehova anamulamulira, ndipo anamwalira ali m’phirimo. Anamwalira m’chaka cha 40 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachisanu, pa tsiku loyamba la mweziwo.+
50 Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake.