17 Kenako Elisa anayamba kupemphera+ kuti: “Inu Yehova, m’tseguleni maso+ chonde kuti aone.” Nthawi yomweyo Yehova anatsegula maso a mtumiki uja, moti anaona kuti dera lonse lamapiri kuzungulira Elisa+ linadzaza ndi mahatchi ndi magaleta ankhondo+ oyaka moto.