6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Isiraeli ndiwo anagonjetsa mafumuwa.+ Atatero, Mose mtumiki wa Yehova anapereka dzikoli kwa Arubeni,+ Agadi,+ ndi hafu ya fuko la Manase,+ kuti likhale lawo.
18 Ana a Rubeni, Agadi, ndi hafu ya fuko la Manase amene anali amuna amphamvu,+ onyamula chishango ndi lupanga, odziwa kupinda uta, ndi odziwa kumenya nkhondo, analipo asilikali 44,760.+