-
Ekisodo 26:32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Nsalu imeneyi uipachike pamizati inayi ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyi tikhale tagolide. Mizati imeneyi ikhale pazitsulo zinayi zasiliva zamphako.
-
-
Ekisodo 26:37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Nsalu yotchinga khomo la chihema uipangire mizati isanu ya mtengo wa mthethe yokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyo tikhale tagolide. Ndipo upange zitsulo zamkuwa zisanu zamphako zokhazikapo mizatiyo.
-