18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+
8 Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbewu yako yobwera pambuyo pako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+