Masalimo
5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+
Kumbukirani zozizwitsa zake ndi zigamulo zotuluka m’kamwa mwake,+
6 Inu mbewu ya Abulahamu mtumiki wake,+
Inu ana a Yakobo, osankhidwa mwapadera.+
8 Wakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+
Wakumbukira lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,+
9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+
Ndi lonjezo limene analumbira kwa Isaki,+
10 Lonjezo limeneli analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,
Monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,+
11 Pamene anati: “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+
Kuti likhale gawo la cholowa chako.”+
12 Pamene ananena zimenezi, n’kuti iwo ali ochepa.+
N’kuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo m’dzikolo.+
13 Iwo anapitiriza kuyendayenda pakati pa mitundu yosiyanasiyana,+
Anali kuchoka mu ufumu wina ndi kupita kukakhala ndi anthu a mtundu wina.+
14 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awachitire zachinyengo,+
Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+
15 Iye anati: “Anthu inu musakhudze odzozedwa anga,+
Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+
16 Iye anadzetsa njala yaikulu m’dzikomo,+
Ndipo anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati.+
17 Mulungu anatsogoza munthu kuti anthu akewo abwere pambuyo pake,
Anatumiza Yosefe amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+
18 Kumeneko anasautsa mapazi ake ndi matangadza,+
Anam’manga ndi maunyolo.+
Kufikira pamene lonjezo la Mulungu linakwaniritsidwa.+
20 Mfumu inalamula kuti amutulutse m’ndende.+
Wolamulira mitundu ya anthu analamula kuti Yosefe amasulidwe.
21 Anamuika kukhala mkulu woyang’anira banja lake,+
Komanso wolamulira chuma chake chonse.+
22 Anamupatsa ulamuliro womanga kalonga aliyense wa mfumu,+
Komanso kuphunzitsa zinthu za nzeru anthu achikulire.+
24 Mulungu anachititsa anthu ake kuberekana,+
Ndipo pang’onopang’ono anawasandutsa anthu amphamvu kuposa adani awo.+
25 Analola adaniwo kusintha mitima yawo ndi kudana ndi anthu ake,+
Anawalola kuchitira atumiki ake zachinyengo.+
31 Analamula kuti pagwe tizilombo touluka toyamwa magazi,+
Komanso ntchentche zoluma m’madera awo onse.+
36 Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa m’dziko lawo,+
Chiyambi cha mphamvu zawo zonse zobereka.+
37 Ndiyeno anayamba kuwatulutsa atatenga siliva ndi golide.+
Pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.
41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+
Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa m’dera lopanda madzi.+
42 Iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+