Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 6:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Ndiyeno Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene analumbirira makolo ako Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsa,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yooneka bwino imene sunamange ndiwe,+

  • Yoswa 11:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Chotero Yoswa analanda dziko lonse monga mmene Yehova analonjezera Mose.+ Ndiyeno Yoswa anapereka dzikolo kwa Aisiraeli monga cholowa chawo, malinga ndi magawo awo potsata mafuko awo.+ Ndipo dziko lonse linakhala bata, lopanda nkhondo.+

  • Yoswa 21:43
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Choncho Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,+ ndipo iwo analanda+ dzikolo n’kumakhalamo.

  • Nehemiya 9:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Pamenepo munawapatsa maufumu+ ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo chigawo ndi chigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ dziko la mfumu ya Hesiboni+ ndi dziko la Ogi+ mfumu ya Basana.+

  • Salimo 78:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,+

      Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,+

      Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo.+

  • Salimo 135:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Dziko lawo analipereka kukhala cholowa,+

      Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+

  • Machitidwe 7:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Ndipo makolo athu amene anachilandira kwa makolo awo, analowa nacho limodzi ndi Yoswa,+ m’dziko limene linali m’manja mwa anthu a mitundu ina+ amene Mulungu anawapitikitsa pamaso pa makolo athu.+ Chihemacho chinakhala m’dziko limeneli mpaka m’masiku a Davide.

  • Machitidwe 13:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Ndipo atawononga mitundu 7 m’dziko la Kanani, anagawa dzikolo kwa Aisiraeli mwa kuchita maere.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena