14Limeneli ndilo dziko limene ana a Isiraeli anatenga monga cholowa chawo m’dziko la Kanani.+ Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mafuko a makolo a ana a Isiraeli, ndiwo anagawa dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+
16Malire a gawo+ la ana a Yosefe+ anayambira kumtsinje wa Yorodano+ kufupi ndi Yeriko kukafika kumadzi a Yeriko chakum’mawa, mpaka kuchipululu chochokera ku Yeriko kukafika kudera lamapiri la Beteli.+
17Fuko la Manase, mwana woyamba wa Yosefe,+ linapatsidwa gawo lake.+ Makiri+ mwana woyamba wa Manase,+ bambo wake wa Giliyadi,+ anali mwamuna wamphamvu pankhondo,+ ndipo gawo lake linali Giliyadi+ ndi Basana.