25 Yerobowamu ndiye anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kunyanja ya Araba.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri amene anachokera ku Gati-heferi.+