Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 26:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 “Upange nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi upetepo akerubi.+

  • Ekisodo 36:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kenako anapanga nsalu yotchinga+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pansaluyi anapetapo akerubi.+

  • Ekisodo 40:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Mkati mwake, udzaikemo likasa la umboni+ ndi kutchinga kumene kuli Likasalo ndi nsalu.+

  • Levitiko 16:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni m’bale wako, kuti asamalowe konse m’malo oyera+ kuseri kwa nsalu yotchinga,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, kuopera kuti angafe,+ chifukwa ine ndidzaonekera mu mtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+

  • Numeri 3:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Ntchito yawo+ inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ndi ziwiya+ za m’malo oyerawo zimene anali kutumikira nazo, ndiponso nsalu yotchinga,+ komanso ntchito zonse zokhudza utumikiwu.

  • Aheberi 9:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena