Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa zam’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

      “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.+

  • Levitiko 27:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “‘Ngati munthu watenga munthu mnzake, nyama kapena munda wake n’kuupatula kuti ukhale woyera kwa Yehova kwamuyaya,* kapena akapereka munthuyo, nyama kapena munda kwa Mulungu kuti auwononge,+ sungagulitsidwe kapena kuwomboledwa.+ Munthu, nyama kapena munda umenewo ndi wopatulika koposa. Zimenezi ndi za Yehova.

  • Levitiko 27:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 “‘Chakhumi* chilichonse+ cha zinthu za m’dzikolo, kaya ndi zokolola m’munda kapena zipatso za m’mitengo, ndi cha Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova.

  • Numeri 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mphatso zonse za ana a Isiraeli, limodzi ndi nsembe zawo zonse zoweyula*+ zimene azipereka monga zopereka zawo,+ zizikhala zako. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna, limodzi ndi ana ako aakazi.+ Zikhale gawo lanu mpaka kalekale. Aliyense wa m’nyumba yako amene ndi wosadetsedwa azidya nawo.+

  • Numeri 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Lankhula ndi Alevi, uwauze kuti, ‘Muzilandira kwa ana a Isiraeli chakhumi chimene ndakupatsani monga cholowa+ chanu. Ndipo pachakhumi chimene muzilandiracho, muziperekapo chopereka chanu kwa Yehova, chakhumi cha chakhumicho.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena