Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 14:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Ndipo adalitsike Mulungu Wam’mwambamwamba,+

      Amene wapereka okupondereza m’manja mwako!”+

      Pamenepo, Abulamu anamupatsa iye chakhumi cha zilizonse.+

  • Genesis 28:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatsa, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi chake.”+

  • Numeri 18:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 “Kunena za ana a Levi, iwo ndawapatsa chakhumi+ chilichonse mu Isiraeli monga cholowa chawo chifukwa cha utumiki wawo umene akuchita, utumiki wa pachihema chokumanako.

  • Numeri 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Lankhula ndi Alevi, uwauze kuti, ‘Muzilandira kwa ana a Isiraeli chakhumi chimene ndakupatsani monga cholowa+ chanu. Ndipo pachakhumi chimene muzilandiracho, muziperekapo chopereka chanu kwa Yehova, chakhumi cha chakhumicho.+

  • Deuteronomo 12:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Nsembe zanu zopsereza+ ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera m’manja mwanu,+ nsembe zanu za lonjezo,+ nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ng’ombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzazibweretsa kumalo amenewo.

  • Deuteronomo 14:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Usalephere kupereka chakhumi cha mbewu zako zonse zokolola m’munda mwako chaka ndi chaka.+

  • 2 Mbiri 31:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ana a Isiraeli+ atangomva mawuwo, anawonjezera zipatso zoyambirira zimene ankapereka za mbewu,+ vinyo watsopano,+ mafuta,+ uchi,+ ndi zokolola zonse zakumunda+ ndipo anabweretsa chakhumi cha zonsezi chochuluka zedi.+

  • Nehemiya 13:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Anthu onse a mu Yuda anabweretsa kumalo osungira zinthu+ chakhumi+ cha mbewu,+ cha vinyo watsopano+ ndiponso cha mafuta.+

  • Malaki 3:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Bweretsani gawo limodzi mwa magawo 10 alionse a zinthu zanu+ n’kuziika mosungiramo zinthu zanga, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya.+ Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi,+ kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba+ ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira,”+ watero Yehova wa makamu.

  • Luka 11:42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 42 Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumapereka chakhumi+ cha timbewu ta minti ndi ta luwe, ndi cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse. Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unalidi udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simunayenera kusiya zinazo.+

  • Aheberi 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Zoonadi, amuna ochokera mwa ana aamuna a Levi,+ amene amalandira udindo wa unsembe, amalamulidwa kulandira zakhumi+ kuchokera kwa anthu+ malinga ndi Chilamulo. Izi zikutanthauza kuti, amalandira zakhumizo kuchokera kwa abale awo, ngakhale kuti abale awowo anachokera m’chiuno mwa Abulahamu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena