28“Koma iwe patula Aroni m’bale wako pamodzi ndi ana ake pakati pa ana a Isiraeli, ndipo Aroniyo+ atumikire monga wansembe wanga pamodzi ndi ana akewo,+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara ndi Itamara.+
5 Pakuti iye ndi amene Yehova Mulungu wako wam’sankha pakati pa mafuko anu onse, kuti iye pamodzi ndi ana ake aimirire ndi kutumikira m’dzina la Yehova nthawi zonse.+