-
Deuteronomo 13:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndipo mneneri+ kapena wolota malotoyo muzimupha,+ chifukwa walankhula mopandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani m’dziko la Iguputo ndi kukuwombolani m’nyumba yaukapolo. Munthu ameneyo walankhula zimenezo kuti akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuyendamo.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+
-
-
2 Samueli 7:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Ndi mtundu uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu munawawombola monga anthu anu+ ndi kudzipangira dzina,+ amene munawachitira zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha?+ Munapitikitsa mitundu ina ndi milungu yawo, chifukwa cha anthu anu amene munawawombola+ nokha kuchokera ku Iguputo.
-