7 Pakuti ndi mtundu winanso uti wamphamvu+ umene milungu yake ili pafupi nawo, monga mmene Yehova Mulungu wathu alili pafupi ndi ife, tikamaitanira pa iye+ nthawi zonse?
21 Ndi mtundu winanso uti padziko lapansi umene ungafanane ndi mtundu wa anthu anu Aisiraeli,+ amene inu Mulungu woona munawawombola monga anthu anu,+ ndi kudzipangira dzina mwa kuchita zinthu zazikulu+ ndi zochititsa mantha, popitikitsa mitundu+ pamaso pa anthu anu amene munawawombola ku Iguputo?