39 Kenako ana a Makiri+ mwana wa Manase, ananyamuka ulendo wopita kumzinda wa Giliyadi. Analanda mzindawo ndi kupitikitsa Aamori amene anali kukhalamo.
31 Mose anapereka hafu ya dera la Giliyadi, Asitaroti,+ Edirei,+ ndi mizinda ya ufumu wa Ogi m’dziko la Basana kwa ana a Makiri,+ mwana wa Manase. Anapereka dzikoli kwa hafu ya ana a Makiri potsata mabanja awo.
4 Iye anadzakhala ndi ana 30 aamuna amene anali kuyenda pa abulu 30,+ ndipo iwo anali ndi mizinda 30. Mizinda imeneyi ikutchedwabe kuti Havoti-yairi*+ kufikira lero, ndipo ili m’dziko la Giliyadi.