Genesis 9:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake. Ekisodo 20:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 “Usaphe munthu.*+ Numeri 35:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+ Mateyu 5:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu.+ Aliyense amene wapha mnzake+ wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ Aroma 13:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,+ Usabe,+ Usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+
6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake.
21 kapena ngati wam’menya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye n’kumupha, wopha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wakupha munthu. Wobwezera magazi aphe wakupha munthuyo akangom’peza.+
21 “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu.+ Aliyense amene wapha mnzake+ wapalamula mlandu wa kukhoti.’+
9 Chifukwa malamulo onena kuti, “Usachite chigololo,+ Usaphe munthu,+ Usabe,+ Usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili m’mawu awa akuti, “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+