Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 20:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Usaphe munthu.*+

  • Numeri 35:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Mizindayo ikakhale kothawirako munthu wopha mnzake amene akuthawa wobwezera magazi,+ kuti amene wapha mnzakeyo asaphedwe kufikira ataima pamaso pa oweruza kuti aweruzidwe.+

  • Numeri 35:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 “‘Aliyense wopezeka kuti wapha munthu,+ atatsimikiziridwa ndi mboni,+ aphedwe. Koma umboni wa munthu mmodzi si wokwanira kuti munthu aphedwe.

  • Deuteronomo 19:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Akapanda kutero, wobwezera magazi+ angathamangitse wopha munthuyo ndi kum’peza, chifukwa mtunda ndi wautali. Pamenepo angamukanthe ndi kumupha chifukwa chakuti mtima wake ndi wodzaza ndi ukali, ngakhale kuti wopha mnzake mwangoziyo sanayenere kufa+ chifukwa sanali kudana naye.

  • 2 Samueli 4:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiye kuli bwanji pamene anthu oipa+ apha munthu wolungama pabedi m’nyumba yake? Kodi sindiyenera kufuna magazi ake m’manja mwanu+ ndi kukuchotsani padziko?”+

  • Mateyu 24:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu+ chidzaonekera kumwamba. Ndiyeno mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni,+ ndipo adzaona Mwana wa munthu akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.+

  • Chivumbulutso 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena