6 Akapanda kutero, wobwezera magazi+ angathamangitse wopha munthuyo ndi kum’peza, chifukwa mtunda ndi wautali. Pamenepo angamukanthe ndi kumupha chifukwa chakuti mtima wake ndi wodzaza ndi ukali, ngakhale kuti wopha mnzake mwangoziyo sanayenere kufa+ chifukwa sanali kudana naye.