Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Iwe usanafike, ndidzachititsa anthu kumva za ine+ ndipo adzanjenjemera. Ndidzasokoneza anthu onse amene udzawapeze. Adani ako onse adzachita mantha ndipo adzathawa.*+

  • Deuteronomo 2:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Lero ndichititsa anthu a mitundu ina okhala pansi pa thambo, amene adzamva za inu, kuchita nanu mantha kwambiri ndi kuyamba kukuopani. Chifukwa cha inu, iwo adzanthunthumira ndi kumva zopweteka zofanana ndi zowawa za pobereka.’+

  • Yoswa 2:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Ndipo iye anauza amunawo kuti: “Ndikudziwa kuti Yehova akupatsani ndithu dziko lino.+ Ife tagwidwa ndi mantha chifukwa cha inu,+ ndipo anthu a dziko lino ataya mtima chifukwa chokuopani.+

  • Yoswa 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena