Yoswa
5 Mafumu onse a Aamori+ amene anali kutsidya la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, ndi mafumu onse a Akanani+ amene anali m’mphepete mwa nyanja, anamva zakuti Yehova anaphwetsa madzi a mtsinje wa Yorodano pamaso pa ana a Isiraeli kufikira atawoloka. Atamva zimenezo, mitima yawo inasungunuka ndi mantha,+ moti anatheratu mphamvu poopa ana a Isiraeli.+
2 Pa nthawi imeneyo, Yehova anauza Yoswa kuti: “Panga timipeni tamiyala kuti udule khungu+ la ana a Isiraeli kachiwiri.” 3 Chotero Yoswa anapanga timipeni tamiyala, ndipo anadula khungu la ana a Isiraeli. Zimenezi zinachitikira ku Gibeyati-haaraloti.+ 4 Yoswa anadula khungu la ana a Isiraeliwo chifukwa chakuti anthu onse amene anatuluka mu Iguputo, amuna onse otha kupita kunkhondo, anali atafera+ m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo. 5 Anthu onse amene anatuluka mu Iguputo anali odulidwa. Koma onse amene anabadwira m’chipululu pa ulendo wochokera ku Iguputo, sanadulidwe. 6 Ana a Isiraeliwo anayenda m’chipululu zaka 40,+ mpaka amuna onse otha kupita kunkhondo amene anatuluka mu Iguputo atatha, amene sanamvere mawu a Yehova. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 7 Iye analowetsa m’dzikomo ana awo m’malo mwa makolowo.+ Ana amenewa Yoswa anawadula khungu, chifukwa sanadulidwe pa nthawi imene anali pa ulendo.
8 Atamaliza kuchita mdulidwe pamtundu wonsewo, anthuwo anakhala m’malo awo mumsasa mpaka atachira.+
9 Kenako Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndachotsa chitonzo cha Iguputo pa inu.”+ Chotero malowo anayamba kuwatchula kuti Giligala,+ kufikira lero.
10 Ana a Isiraeliwo anakhalabe ku Giligala. Anachita pasika madzulo pa tsiku la 14 la mweziwo,+ ali m’chipululu cha Yeriko. 11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za m’dzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda chofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene ana a Isiraeli anadya zokolola za m’dzikomo. Kuyambira pamenepo, mana sanagwenso pakati pa ana a Isiraeli.+ Chotero, chaka chimenechi n’chimene iwo anayamba kudya zokolola za m’dziko la Kanani.+
13 Tsiku lina Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima potero patsogolo pake, ali ndi lupanga m’dzanja lake.+ Pamenepo Yoswa anayandikira munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?” 14 Munthuyo anayankha kuti: “Iyayi, koma ine pokhala kalonga wa gulu lankhondo la Yehova, tsopano ndabwera.”+ Yoswa atamva mawu amenewo, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+ ndipo anamuuza kuti: “Lankhulani mbuyanga kwa kapolo wanu.” 15 Ndiyeno kalonga wa gulu lankhondo la Yehovayo anauza Yoswa kuti: “Vula nsapato zako, chifukwa malo amene waimapowo ndi oyera.” Nthawi yomweyo, Yoswa anavula nsapato zake.+