25 Ndiyeno zinachitika kuti usiku womwewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono yamphongo ya bambo ako, ng’ombe yachiwiri yazaka 7 ija. Kenako ugwetse guwa lansembe la Baala+ la bambo ako ndipo udule mzati wopatulika umene uli pafupi ndi guwalo.+