14 Pakuti moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake, chifukwa m’magazimo ndi mmene muli moyo. N’chifukwa chake ndauza ana a Isiraeli kuti: “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake.+ Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.”+