30 Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake m’manja mwa Isiraeli. Choncho Aisiraeli anapha anthu onse a mumzindawo ndi lupanga, ndipo anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka. Mfumu ya ku Libina anaichita zofanana ndi zomwe anachita mfumu ya ku Yeriko.+