Ekisodo 12:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo. Yoswa 2:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Tikubwera ndithu m’dziko muno! Chingwe chofiira ichi uchimangirire pawindo limene watitulutsirapo. Bambo ako ndi mayi ako, abale ako ndi alongo ako, ndi onse a m’nyumba ya bambo ako, uwasonkhanitse kuti adzakhale m’nyumba mwako.+ Oweruza 6:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Pamenepo iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ mundisonyeze chizindikiro kuti nditsimikize kuti ndinudi amene mukulankhula nane.+
13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalamo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo ndi kukupitirirani,+ choncho mliri sudzakugwerani ndi kukuwonongani pamene ndikukantha dziko la Iguputo.
18 Tikubwera ndithu m’dziko muno! Chingwe chofiira ichi uchimangirire pawindo limene watitulutsirapo. Bambo ako ndi mayi ako, abale ako ndi alongo ako, ndi onse a m’nyumba ya bambo ako, uwasonkhanitse kuti adzakhale m’nyumba mwako.+
17 Pamenepo iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima,+ mundisonyeze chizindikiro kuti nditsimikize kuti ndinudi amene mukulankhula nane.+