36 Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli m’mbali mwa chigwa cha Arinoni, ndiponso kuchokera kumzinda wa m’chigwa mpaka ku Giliyadi, panalibe mzinda womwe unali wa malinga aatali kwambiri kwa ife.+ Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife.
26 Pamene Aisiraeli anali kukhala ku Hesiboni ndi m’midzi yake yozungulira,+ ku Aroweli+ ndi m’midzi yake yozungulira ndi m’mizinda yonse ya m’gombe la Arinoni kwa zaka 300, n’chifukwa chiyani simunawalande mizindayo pa nthawi imeneyo?+