11 Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kum’mawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akagunde malo otsetsereka a kum’mawa kwa nyanja ya Kinereti.*+
17 Ndinawapatsa Araba, Yorodano ndi tsidya lake la kum’mawa, kuchokera ku Kinereti*+ mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere+ imene ili m’munsi mwa Pisiga,+ kotulukira dzuwa.