-
Numeri 33:54Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
54 Mukagawire dzikolo kwa mabanja anu monga cholowa chanu mwa kuchita maere.+ Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo.+ Malo alionse amene maere akagwere banja, akapatsidwe kwa banjalo.+ Mukagawane malowo potsata mafuko a makolo anu.+
-