Genesis 24:54 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 54 Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko ndi kudzuka m’mawa. Kenako mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+ Aroma 12:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Gawanani ndi oyera malinga ndi zosowa zawo.+ Khalani ochereza.+ Aheberi 13:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Musaiwale kuchereza alendo,+ pakuti potero, ena anachereza angelo mosadziwa.+
54 Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko ndi kudzuka m’mawa. Kenako mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuyanga.”+