-
Yoswa 13:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 (Dera loyambira kukamtsinje kotuluka mu Nailo kum’mawa kwa Iguputo, kukafika kumpoto kumalire ndi Ekironi,+ ankalitcha dziko la Akanani.)+ Madera a Afilisitiwa akulamulidwa ndi olamulira ogwirizana asanu.+ Maderawo ndi Gaza,+ Asidodi,+ Asikeloni,+ Gati+ ndi Ekironi,+ komanso Aavi+ akukhala komweko.
-
-
1 Samueli 6:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Chiwerengero cha mbewa zoyenda modumpha zagolide chinali chofanana ndi mizinda yonse ya Afilisiti ya olamulira asanu ogwirizana, kuyambira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mpaka ku mudzi wopanda mpanda.
Mwala waukulu umene anakhazikapo likasa la Yehova ndiwo mboni mpaka lero m’munda wa Yoswa, amene kwawo kunali ku Beti-semesi.
-