16 Ndiyeno ana a munthu wa mtundu wachikeni,+ amene anali apongozi ake a Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi ana a Yuda kukalowa m’chipululu cha Yuda, chimene chili kum’mwera kwa Aradi.+ Motero iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+
11 Zili choncho, Hiberi+ Mkeni anapatukana ndi Akeni,+ ana a Hobabu mpongozi wa Mose,+ ndipo anamanga hema wake pafupi ndi mtengo waukulu ku Zaananimu, ku Kedesi.