Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndipo Baraki anasonkhanitsa pamodzi fuko la Zebuloni+ ndi fuko la Nafitali ku Kedesi, moti amuna 10,000 anam’tsatira,+ ndipo Debora nayenso anapita nawo.

  • Oweruza 6:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Iye anatumiza mithenga+ m’dera lonse la fuko la Manase, ndipo anthu a m’fuko limeneli nawonso anasonkhana pamodzi n’kuyamba kumutsatira. Anatumizanso mithenga m’madera onse a mafuko a Aseri, Zebuloni ndi Nafitali, ndipo nawonso anabwera kudzakumana naye.

  • 1 Mbiri 12:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 A fuko la Zebuloni,+ onse oyenerera kupita kunkhondo, kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ndi zida zawo zonse zankhondo, analipo 50,000. Popita kwa Davide, iwo sanapite ndi mitima iwiri.

  • Salimo 68:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Pali fuko laling’ono la Benjamini limene likugonjetsa anthu,+

      Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi makamu awo amene akufuula,

      Palinso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafitali.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena