20 Ndipo magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Atatero ananyamulanso miyuni ndi dzanja lawo lamanzere ndipo malipenga anali m’dzanja lawo lamanja, n’kuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!”