2 “Utume amuna kuti akazonde dziko la Kanani limene ndikulipereka kwa ana a Isiraeli.+ Pa fuko lililonse utume mwamuna mmodzi, amene ali mtsogoleri+ wa fukolo.”
2 Tsopano Yoswa anatumiza amuna ena kuchokera ku Yeriko kupita ku Ai,+ pafupi ndi Beti-aveni,+ kum’mawa kwa Beteli.+ Iye anawauza kuti: “Pitani kumeneko, mukazonde dzikolo.” Amunawo anapita, n’kukazonda dziko la Ai.+