-
Esitere 8:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiyeno Moredekai anachoka pamaso pa mfumu atavala chovala chachifumu+ cha buluu ndi nsalu yoyera. Analinso atavala chisoti chachikulu chachifumu chagolide, mkanjo wa nsalu yabwino kwambiri yaubweya wa nkhosa+ wonyika mu utoto wofiirira.+ Ndipo mumzinda wa Susani munamveka kufuula kwa chisangalalo ndi kukondwera.+
-
-
Yeremiya 10:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Siliva wosulidwa kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.+ Zonsezi zimakonzedwa mwaluso, ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo. Mafanowo amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Nawonso angokhala ntchito ya amisiri aluso.+
-