Yoswa 19:47 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 47 Gawo la ana a Dani linawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo n’kupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga n’kuyamba kukhalamo ndipo anautcha Lesemu Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+ Oweruza 18:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndipo m’masiku amenewo fuko la Dani+ linali kufuna cholowa chake kuti likakhale kumeneko, chifukwa mpaka pa nthawi imeneyi linali lisanalandirebe cholowa pakati pa mafuko onse a Isiraeli.+
47 Gawo la ana a Dani linawachepera,+ choncho anapita kukachita nkhondo ku Lesemu.+ Analanda mzindawo n’kupha anthu ake ndi lupanga. Kenako anautenga n’kuyamba kukhalamo ndipo anautcha Lesemu Dani, potengera dzina la kholo lawo Dani.+
18 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndipo m’masiku amenewo fuko la Dani+ linali kufuna cholowa chake kuti likakhale kumeneko, chifukwa mpaka pa nthawi imeneyi linali lisanalandirebe cholowa pakati pa mafuko onse a Isiraeli.+