2 Koma Sauli ndi amuna a Isiraeli anasonkhana pamodzi n’kumanga msasa m’chigwa cha Ela,+ ndipo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi Afilisiti.
50 Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+