Miyambo 14:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+ koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.+ Miyambo 24:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Nzeru zimamanga banja la munthu,+ ndipo kuzindikira kumachititsa kuti lilimbe kwambiri.+ Miyambo 31:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+ ndipo lamulo la kukoma mtima kosatha lili palilime lake.+