Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 13:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Koma mkazi wakeyo anati: “Yehova akanakhala kuti akufuna kutipha, sakanalandira m’manja mwathu nsembe yopsereza ndi nsembe yathu yambewu.+ Komanso sakanationetsa ndi kutiuza zinthu zonsezi.”+

  • 1 Samueli 25:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Choncho musalole kuti zimenezi zikhale zokuvutitsani chikumbumtima ndi zokhumudwitsa mumtima mwanu mbuyanga, mwa kukhetsa magazi popanda chifukwa+ ndi kudzipulumutsa nokha ndi dzanja lanu.+ Mukatero, Yehova adzakuchitirani zabwino mbuyanga, ndipo mudzandikumbukire+ ine kapolo wanu wamkazi.”

  • 2 Samueli 20:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndiyeno mkazi wina wanzeru+ mumzindawo anayamba kufuula kuti: “Tamverani amuna inu, tamverani! Chonde muuzeni Yowabu kuti abwere pafupipa kuti ndilankhule naye.”

  • Esitere 5:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ngati mungandikomere mtima mfumu+ ndipo ngati zingakukomereni kuchita zimene ndapempha n’kundipatsa zimene ndikufuna, inu mfumu ndi Hamani mubwere kuphwando limene ndidzakukonzerani mawa. Ndipo mawa ndidzanena pempho langa monga mmene inu mfumu mwanenera.”+

  • Salimo 68:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yehova wapereka lamulo,+

      Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.+

  • Miyambo 31:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Mawu a Mfumu Lemueli, uthenga wamphamvu+ umene mayi ake anamupatsa pomuphunzitsa:+

  • Machitidwe 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Mwamuna ameneyu anayamba kulankhula molimba mtima musunagoge. Tsopano Purisikila ndi Akula+ atamumvetsera, anamutenga ndi kumufotokozera njira ya Mulungu molondola.

  • Tito 2:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Chimodzimodzinso akazi achikulire.+ Akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza. Asakhale amiseche,+ kapena akapolo a vinyo wambiri, koma akhale aphunzitsi a zinthu zabwino,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena