26 Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+