7 Aheberi ena mpaka anawoloka Yorodano+ kupita m’dera la Gadi+ ndi la Giliyadi. Koma Sauli anali adakali ku Giligala, ndipo anthu onse anali kunjenjemera pamene anali kum’tsatira.+
2 Pa nthawiyi Sauli anali kukhala kunja kwa mzinda wa Gibeya+ pansi pa mtengo wa makangaza* umene uli ku Migironi. Iye anali ndi amuna pafupifupi 600.+