23 Pamene anali kulankhula ndi asilikaliwo, anangoona ngwazi ija yatulukira kuchokera pakati pa asilikali a Afilisiti. Dzina la ngwaziyo linali Goliyati,+ Mfilisiti wa ku Gati.+ Iye anayamba kulankhula mawu omwe aja amene analankhula poyamba,+ moti Davide anamva nawo.