Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Oweruza 14:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Pamenepo Samisoni anapita ku Timuna+ pamodzi ndi bambo ndi mayi ake. Atafika m’minda ya mpesa ya ku Timuna, anakumana ndi mkango wamphamvu umene unayamba kubangula utamuona.

  • Miyambo 30:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Mkango, umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire ndiponso umene suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo,+

  • Yesaya 31:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Mkango umalira moopseza, ngakhale mkango wamphamvu,+ poteteza nyama imene wagwira. Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse, ngakhale umve mawu awo suchita mantha ndipo ngakhale azichita phokoso suopa. M’njira yomweyo, Yehova wa makamu adzatsika kuti achite nkhondo poteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake laling’ono.+

  • Amosi 3:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 “Yehova wanena kuti, ‘Monga mmene m’busa amapulumutsira ziboda ziwiri za chiweto ndi kachidutswa ka khutu m’kamwa mwa mkango,+ nawonso ana a Isiraeli amene akukhala m’Samariya pamipando yapamwamba+ ndi kugona pamabedi a ku Damasiko+ adzapulumuka ochepa chabe m’manja mwa adani awo.’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena