7 Choncho asilikali a Yowabu,+ Akereti,+ Apeleti+ ndi amuna onse amphamvu anayamba kumuthamangitsa. Iwo anatuluka mu Yerusalemu ndi kuthamangitsa Sheba mwana wa Bikiri.
10 Tsopano otsatirawa ndiwo atsogoleri a amuna amphamvu+ a Davide omwe anali kulimbikitsa nawo ufumu wake mwamphamvu pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu malinga ndi mawu a Yehova+ okhudza Isiraeli.