3 Koma Yowabu anati: “Yehova awonjezere anthu ake kuwirikiza nthawi 100 pa chiwerengero chawo.+ Koma kodi mbuyanga mfumu, anthu onsewa si anu komanso si atumiki anu? Nanga n’chifukwa chiyani mbuyanga mukufuna kuchita zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mukufuna kupalamulitsa Isiraeli?”