1 Mbiri
21 Tsopano Satana anayamba kulimbana ndi Isiraeli polimbikitsa+ Davide kuti awerenge Aisiraeli. 2 Chotero Davide anauza Yowabu+ ndi atsogoleri a anthu kuti: “Pitani mukawerenge+ Aisiraeli kuyambira ku Beere-seba+ mpaka ku Dani,+ ndipo mubweretse chiwerengero chawo kwa ine kuti ndidziwe kuchuluka kwawo.”+ 3 Koma Yowabu anati: “Yehova awonjezere anthu ake kuwirikiza nthawi 100 pa chiwerengero chawo.+ Koma kodi mbuyanga mfumu, anthu onsewa si anu komanso si atumiki anu? Nanga n’chifukwa chiyani mbuyanga mukufuna kuchita zimenezi?+ N’chifukwa chiyani mukufuna kupalamulitsa Isiraeli?”
4 Koma mawu a mfumu+ anaposa mawu a Yowabu moti Yowabu anachoka pamaso pa mfumu+ n’kuyenda mu Isiraeli yense. Kenako anabwerera ku Yerusalemu.+ 5 Atafika kumeneko, Yowabu anapereka chiwerengero chonse cha anthu kwa Davide. Aisiraeli onse analipo 1,100,000, amuna ogwira lupanga,+ ndipo amuna a Yuda ogwira lupanga analipo 470,000. 6 Koma Yowabu sanawerenge+ a fuko la Levi+ ndi la Benjamini, chifukwa anali ataipidwa ndi mawu a mfumu.
7 Zinthu zimenezi zinali zoipa pamaso pa Mulungu woona,+ ndipo anapha Aisiraeli. 8 Davide ataona zimenezo, anauza Mulungu woona kuti: “Ndachimwa+ kwambiri pochita zimene ndachitazi. Tsopano, chonde, khululukani cholakwa cha ine mtumiki wanu,+ pakuti ndachita chinthu chopusa kwambiri.”+ 9 Pamenepo Yehova analankhula kwa Gadi,+ wamasomphenya wa Davide+ kuti: 10 “Pita, ukauze Davide kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndaika zilango zitatu pamaso pako.+ Sankha wekha chimodzi mwa zitatuzi chimene ukufuna kuti ndikuchitire.”’”+ 11 Choncho Gadi anapita kwa Davide+ ndi kumuuza kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Sankhapo chimodzi: 12 Zaka zitatu za njala+ kapena miyezi itatu yoti adani anu akuseseni+ ndi kukuphani ndi lupanga lawo, kapenanso masiku atatu a lupanga la Yehova,+ lomwe ndi mliri+ umene udzagwe m’dziko lanu mpaka mngelo wa Yehova atasakaza+ madera onse a Isiraeli.’ Ndiye tandiuzani zoti ndikayankhe kwa Amene wanditumayo.” 13 Atamva zimenezo, Davide anauza Gadi kuti: “Zimenezi zikundisautsa kwambiri. Chonde, ndilangidwe ndi Yehova,+ pakuti chifundo chake n’chochuluka,+ koma ndisalangidwe ndi munthu.”+
14 Pamenepo Yehova anagwetsa mliri+ mu Isiraeli, moti mu Isiraeli munafa anthu 70,000.+ 15 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu woona anatumiza mngelo ku Yerusalemu kuti akawononge mzindawo.+ Mngeloyo atangoyamba kuwononga, Yehova anaona zimenezo ndi kumva chisoni chifukwa cha tsokalo,+ choncho anauza mngelo amene anali kuwonongayo kuti: “Basi pakwanira!+ Tsitsa dzanja lako tsopano.” Pa nthawiyi, mngelo wa Yehova uja anali ataimirira pafupi ndi malo opunthira mbewu a Orinani+ Myebusi.+
16 Davide atakweza maso ake, anaona mngelo wa Yehova+ ataima m’malere, pakati padziko lapansi ndi kumwamba. Mngeloyo anali atagwira lupanga+ n’kuloza nalo Yerusalemu. Nthawi yomweyo, Davide ndi akulu amene anali naye, atavala ziguduli,*+ anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 17 Kenako Davide anauza Mulungu woona kuti: “Kodi si ine amene ndinalamula kuti awerenge anthu? Ndipo kodi si ine ndachimwa ndi kuchitadi cholakwa?+ Nanga nkhosazi+ zalakwa chiyani? Chonde Yehova Mulungu wanga, dzanja lanu likhale pa ine ndi panyumba ya bambo anga, koma mliriwu usakhale pa anthu anu.”+
18 Ndiyeno mngelo wa Yehova anauza Gadi+ kuti auze Davide kuti Davideyo apite kumalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, n’kukamanga guwa lansembe la Yehova.+ 19 Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi amene anawanena m’dzina la Yehova.+ 20 Pamene zimenezi zinali kuchitika, Orinani+ anali akupuntha tirigu. Atatembenuka anaona mngelo, ndipo ana ake anayi amene anali naye limodzi anakabisala. 21 Davide uja anakafika kwa Orinani. Ndiye Orinani atakweza maso n’kuona Davide,+ nthawi yomweyo anachoka pamalo opunthira mbewu aja n’kukagwada pamaso pa Davide n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. 22 Kenako Davide anauza Orinani kuti: “Ndipatse malo ako opunthira mbewuwa kuti ndimangirepo Yehova guwa lansembe, kuti mliriwu+ uthe pakati pa anthuwa. Ndikupatsa ndalama+ zake zonse.”+ 23 Koma Orinani anauza Davide kuti: “Ingotengani malowa akhale anu,+ ndipo mbuyanga mfumu chitani chilichonse chimene mukuona kuti n’chabwino. Taonani, ineyo ndipereka ng’ombe+ kuti zikhale nsembe zopsereza ndi chopunthira tirigu+ kuti chikhale nkhuni,+ ndiponso ndipereka tirigu kuti akhale nsembe yambewu. Ndikupereka zonsezi.”+
24 Koma Mfumu Davide inauza Orinani kuti: “Iyayi, ineyo ndigula ndipo ndipereka ndalama zake zonse,+ chifukwa sindingatenge zinthu zako n’kupita nazo kwa Yehova kukapereka nsembe zopsereza popanda kulipira.” 25 Atatero, Davide anapatsa Orinani ndalama za malowo zolemera masekeli* 600 agolide.+ 26 Ndiyeno Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamalopo,+ ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Komanso anaitana pa dzina la Yehova+ yemwe tsopano anamuyankha ndi moto+ wochokera kumwamba umene unafika paguwa lansembe yopsereza. 27 Kenako Yehova analankhula ndi mngelo uja,+ ndipo mngeloyo anabwezera lupanga lake m’chimake. 28 Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pamalo opunthira mbewu a Orinani Myebusi, anapitiriza kuperekera nsembe pamalopo.+ 29 Koma pa nthawiyo, chihema chopatulika cha Yehova chimene Mose anapanga m’chipululu ndi guwa lansembe zopsereza, zinali pamalo okwezeka a ku Gibeoni.+ 30 Davide anali atasiya kupita kumeneko kukafunsira kwa Mulungu, chifukwa anali kuopa+ lupanga la mngelo wa Yehova.