21 Pamenepo Ahitofeli anauza Abisalomu kuti: “Ugone ndi adzakazi a bambo ako+ amene wawasiya kuti azisamalira nyumba.+ Ukatero Aisiraeli onse adzamva kuti wadzinunkhitsa+ pamaso pa bambo ako,+ ndipo manja+ a anthu onse amene ali ndi iwe adzalimba ndithu.”